Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:26

[1] Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,

[2] “Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa? Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?

[3] Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?

[4] Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’

[5] Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe

[6] ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake, pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri. Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.

[7] “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?

[8] Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani? Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani?

[9] Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.

[10] “Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?

[11] Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo; akaona choyipa, kodi sachizindikira?

[12] Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.

[13] “Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,

[14] ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,

[15] udzatukula mutu wako wosachita manyazi; udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.

[16] Udzayiwala ndithu zowawa zako, zidzakhala ngati madzi amene apita kale.

[17] Moyo wako udzawala kupambana usana, ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.

[18] Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo; ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.

[19] Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.

[20] Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza, ndipo adzasowa njira yothawirapo; chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”

Yobu — Chapters