Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:51

[1] “Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.

[2] Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake, kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.

[3] Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.

[4] Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka. Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero. Pamene wabangula, palibe chimene amalephera kuchita.

[5] Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.

[6] Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’ ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’

[7] Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake. Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.

[8] Zirombo zimakabisala ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.

[9] Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake, kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.

[10] Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.

[11] Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula, amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.

[12] Mulungu amayendetsa mitamboyo mozungulirazungulira dziko lonse lapansi kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.

[13] Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu, kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.

[14] “Abambo Yobu, tamvani izi; imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.

[15] Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?

[16] Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo, ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?

[17] Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,

[18] kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo limene ndi lolimba ngati chitsulo?

[19] “Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye; sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.

[20] Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu? Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?

[21] Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa, ndi kunyezimira mlengalenga, kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.

[22] Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto; Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.

[23] Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa; pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.

[24] Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri, kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”

Yobu — Chapters