Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:30

[1] Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

[2] “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama, Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,

[3] nthawi zonse pamene ndili ndi moyo, mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,

[4] pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa, lilime langa silidzayankhula zachinyengo.

[5] Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona; mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.

[6] Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere; chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.

[7] “Mdani wanga akhale ngati woyipa, wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!

[8] Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu achotsa moyo wake?

[9] Kodi Mulungu amamva kulira kwake pamene zovuta zamugwera?

[10] Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse? Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?

[11] “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.

[12] Inu mwadzionera nokha zonsezi. Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?

[13] “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa, cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.

[14] Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo zidzukulu zake zidzasowa zakudya.

[15] Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri, ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.

[16] Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, ndi kukundika zovala ngati mchenga,

[17] zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale, ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.

[18] Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche, ili ngati msasa umene mlonda amamanga.

[19] Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko; akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.

[20] Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula; mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.

[21] Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo imamuchotsa pamalo pake.

[22] Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni, pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.

[23] Mphepoyo imamuwomba ndithu ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”

Yobu — Chapters