Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:26

[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,

[2] “Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri; Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.

[3] Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu; ndikanangopita kumene amakhalako!

[4] Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.

[5] Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha, ndi kulingalira bwino zimene akananena!

[6] Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu? Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.

[7] Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake, ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.

[8] “Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko, ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.

[9] Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko akapita kummwera, sindimuona.

[10] Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.

[11] Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake; ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.

[12] Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.

[13] “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye? Iye amachita chilichonse chimene wafuna.

[14] Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire, ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.

[15] Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake; ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.

[16] Mulungu walefula mtima wanga; Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.

[17] Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima, ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.

Yobu — Chapters