[1] “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
[2] Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
[3] Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
[4] Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
[5] Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
[6] Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
[7] Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
[8] Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso.
[9] Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
[10] Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
[11] Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
[12] “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho, za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
[13] Ndani angasende chikopa chake? Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
[14] Ndani angatsekule kukamwa kwake, pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
[15] Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana;
[16] Mambawo ndi olukanalukana kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
[17] Ndi olumikizanalumikizana; ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
[18] Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali; maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
[19] Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo mumathetheka mbaliwali zamoto.
[20] Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
[21] Mpweya wake umayatsa makala, ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
[22] Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake; aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
[23] Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
[24] Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala, ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
[25] Ngʼonayo ikangovuwuka, ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
[26] Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu, ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
[27] Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
[28] Muvi sungathe kuyithawitsa, miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
[29] Zibonga zimakhala ngati ziputu; imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
[30] Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
[31] Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali, imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
[32] Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
[33] Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, nʼcholengedwa chopanda mantha.
[34] Chimanyoza nyama zina zonse; icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”