[1] “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera? Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
[2] Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere? Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
[3] Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo; pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
[4] Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo; kenaka amachoka ndipo sabwereranso.
[5] “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani amamasula zingwe zake?
[6] Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake, nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
[7] Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda; ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
[8] Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.
[9] “Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone mu gome lako usiku?
[10] Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
[11] Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake? Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
[12] Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako ndi kumuyika ku malo opunthira?
[13] “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira, koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.
[14] Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi ndipo amafundidwa ndi nthaka,
[15] nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa, ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.
[16] Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake; Imayiwala zoti inavutika powabala.
[17] Chifukwa Mulungu anayimana nzeru, simvetsa kanthu kalikonse.
[18] Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga, imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
[19] “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?
[20] Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira, ukali wake nʼkumachititsa mantha?
[21] Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.
[22] Iye sachita mantha, saopa chilichonse; sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.
[23] Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.
[24] Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha; satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.
[25] Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali, kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.
[26] “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako, ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?
[27] Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?
[28] Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku; chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.
[29] Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye; maso ake amachionera patali chinthucho.
[30] Ana ake amayamwa magazi, ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”