Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:30

[1] “Mtima wanga wasweka, masiku anga atha, manda akundidikira.

[2] Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira; maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.

[3] “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna. Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?

[4] Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu; choncho simudzawalola kuti apambane.

[5] Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma, ana ake sadzaona mwayi.

[6] “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense, munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.

[7] Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni; ndawonda ndi mutu womwe.

[8] Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi; anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.

[9] Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo, ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.

[10] “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo, sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.

[11] Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka, pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.

[12] Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana, nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’

[13] Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda, ngati ndiyala bedi langa mu mdima,

[14] ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’

[15] tsono chiyembekezo changa chili kuti? Ndani angaone populumukira panga?

[16] Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse, polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.”

Yobu — Chapters