Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:28

[1] Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!

[2] Monga momwe moto umatenthera tchire ndiponso kuwiritsa madzi, tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu, ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.

[3] Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere, ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.

[4] Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo kapena kuona Mulungu wina wonga Inu, amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.

[5] Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amakumbukira njira zanu. Koma Inu munakwiya, ife tinapitiriza kuchimwa. Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?

[6] Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa, ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo; tonse tafota ngati tsamba, ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.

[7] Palibe amene amapemphera kwa Inu kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu; pakuti mwatifulatira ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.

[8] Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.

[9] Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso musakumbukire machimo athu mpaka muyaya. Chonde, mutiganizire, ife tikupempha, pakuti tonsefe ndi anthu anu.

[10] Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu; ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.

[11] Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani, yatenthedwa ndi moto ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.

[12] Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza? Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?

Yesaya — Chapters