Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:07

[1] Beli wagwada pansi, Nebo wawerama; nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo. Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe. Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.

[2] Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo; sizikutha kupulumutsa katunduyo, izo zomwe zikupita ku ukapolo.

[3] Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo, inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli, Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu, ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.

[4] Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.

[5] “Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani? Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?

[6] Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.

[7] Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.

[8] “Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi, Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.

[9] Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane.

[10] Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

[11] Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa. Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa. Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi; zimene ndafuna ndidzazichitadi.

[12] Ndimvereni, inu anthu owuma mtima, inu amene muli kutali ndi chipulumutso.

[13] Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa; sichili kutali. Tsikulo layandikira ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.

Yesaya — Chapters