Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:02

[1] Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, kuchokera ku chipululu, dziko lochititsa mantha.

[2] Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.

[3] Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.

[4] Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha; chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna chasanduka chinthu choopsa kwa ine.

[5] Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”

[6] Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; “Pita, kayike mlonda kuti azinena zimene akuziona.

[7] Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo ndipo akuyenda awiriawiri, okwera pa bulu kapena okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru kwambiri.”

[8] Ndipo mlondayo anafuwula kuti, “Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera; Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.

[9] Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”

[10] Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu, ine ndikukuwuzani zimene ndamva ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli.

[11] Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”

[12] Mlonda akuyankha kuti, “Kukucha, koma kudanso. Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; ndipo ubwerenso udzafunse.”

[13] Uthenga wonena za Arabiya: Inu anthu amalonda a ku Dedani, amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,

[14] perekani madzi kwa anthu aludzu. Inu anthu a ku Tema perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.

[15] Iwo akuthawa malupanga, lupanga losololedwa, akuthawa uta wokokakoka ndiponso nkhondo yoopsa.

[16] Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.

[17] Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.

Yesaya — Chapters