Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:25

[1] Uthenga wonena za Turo: Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi: pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa ndipo mulibe nyumba kapena dooko. Zimenezi anazimva pochokera ku Kitimu.

[2] Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja, inu amalonda a ku Sidoni, iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.

[3] Pa nyanja zazikulu panabwera tirigu wa ku Sihori; zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda ndi anthu a mitundu ina.

[4] Chita manyazi, iwe Sidimu pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti, “Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana; sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”

[5] Mawuwa akadzamveka ku Igupto, iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.

[6] Wolokerani ku Tarisisi, lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.

[7] Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja, mzinda wakalekale, umene anthu ake ankapita kukakhala ku mayiko akutali?

[8] Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina, mzinda umene amalonda ake ndi akalonga ndi otchuka pa dziko lapansi?

[9] Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi kuti athetse kunyada kwawo ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.

[10] Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo inu anthu a ku Tarisisi, pakuti mulibenso chokutetezani.

[11] Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja ndipo wagwedeza maufumu ake. Iye walamula kuti Kanaani agwetse malinga ake.

[12] Iye anati, “Simudzakondwanso konse, inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa! “Ngakhale muwolokere ku Kitimu, kumeneko simukapezako mpumulo.”

[13] Onani dziko la Ababuloni, anthu amenewa tsopano atheratu! Asiriya asandutsa Turo kukhala malo a zirombo za ku chipululu; anamanga nsanja zawo za nkhondo, anagumula malinga ake ndipo anawasandutsa bwinja.

[14] Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi; chifukwa malinga ako agwetsedwa!

[15] Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:

[16] “Tenga zeze wako uzungulire mzinda, iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika; imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri, kuti anthu akukumbukire.”

[17] Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi.

[18] Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.

Yesaya — Chapters