[1] Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
[2] Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti,
[3] “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
[4] Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti:
[5] “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako.
[6] Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
[7] “ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:
[8] Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
[9] Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
[10] Ine ndinaganiza kuti ndidzapita ku dziko la akufa pamene moyo ukukoma.
[11] Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova, mʼdziko la anthu amoyo, sindidzaonanso mtundu wa anthu kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
[12] Nyumba yanga yasasuka ndipo yachotsedwa. Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga, ngati munthu wowomba nsalu; kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
[13] Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa; koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango, ndipo mwakhala mukundisiya.
[14] Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba, ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula. Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga. Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”
[15] Koma ine ndinganene chiyani? Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi. Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga, ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
[16] Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu. Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu. Munandichiritsa ndi kundikhalitsa ndi moyo.
[17] Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere kuti ndikhale ndi moyo; Inu munandisunga kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko chifukwa mwakhululukira machimo anga onse.
[18] Pakuti akumanda sangathe kukutamandani, akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani. Iwo amene akutsikira ku dzenje sangakukhulupirireni.
[19] Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani, monga mmene ndikuchitira ine lero lino; abambo amawuza ana awo za kukhulupirika kwanu.
[20] Yehova watipulumutsa. Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe masiku onse a moyo wathu mʼNyumba ya Yehova.
[21] Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”
[22] Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”