Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:58

[1] “Tsika, ndi kukhala pa fumbi, iwe namwali, Babuloni; khala pansi wopanda mpando waufumu, iwe namwali, Kaldeya pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera kumugwira mosamala.

[2] Tenga mphero ndipo upere ufa; chotsa nsalu yako yophimba nkhope kwinya chovala chako mpaka ntchafu ndipo woloka mitsinje.

[3] Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.”

[4] Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

[5] “Khala chete, ndipo lowa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya; chifukwa sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.

[6] Ndinawakwiyira anthu anga, osawasamalanso. Ndinawapereka manja mwako, ndipo iwe sunawachitire chifundo. Iwe unachitira nkhanza ngakhale nkhalamba.

[7] Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse ngati mfumukazi.’ Koma sunaganizire zinthu izi kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.

[8] “Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, amene ukukhala mosatekesekawe, umaganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, ndipo ana anga sadzamwalira.’

[9] Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu ngakhale ali ndi amatsenga ambiri ndi mawula amphamvu.

[10] Iwe unkadalira kuyipa kwako ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’

[11] Ngozi yayikulu idzakugwera ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwachotsa; chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa chidzakugwera mwadzidzidzi.

[12] “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako.

[13] Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.

[14] Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa okha ku mphamvu ya malawi a moto. Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.

[15] Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. Onse adzamwazika ndi mantha, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”

Yesaya — Chapters