[1] “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso ndiponso amene mumafunafuna Yehova: Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
[2] taganizani za Abrahamu, kholo lanu, ndi Sara, amene anakubalani. Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana, koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
[3] Yehova adzatonthozadi Ziyoni, ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse; Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni, malo ake owuma ngati munda wa Yehova. Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda ndi kundiyamika.
[4] “Mverani Ine, anthu anga: tcherani khutu, inu mtundu wanga: malangizo adzachokera kwa Ine; cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
[5] Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga. Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga; ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse. Mayiko akutali akundiyembekezera. Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
[6] Kwezani maso anu mlengalenga, yangʼanani pansi pa dziko; mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
[7] “Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi, anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu; musaope kudzudzulidwa ndi anthu kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
[8] Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala; mbozi idzawadya ngati thonje. Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya, chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
[9] Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe, Inu Yehova; dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana, monga nthawi ya mibado yakale. Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe, amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?
[10] Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu, madzi ozama kwambiri aja? Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama, kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
[11] Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa; chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe, chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
[12] Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima. Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa? Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
[13] Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu, amene anayala za mlengalenga ndi kuyika maziko a dziko lapansi. Inu nthawi zonse mumaopsezedwa chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani amene angofuna kukuwonongani. Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
[14] Amʼndende adzamasulidwa posachedwa; sadzalowa mʼmanda awo, kapena kusowa chakudya.
[15] Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
[16] Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa. Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga, ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi, ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
[17] Dzambatuka, dzambatuka! Imirira iwe Yerusalemu. Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo chimene Yehova anakupatsa. Iwe amene unagugudiza chikho chochititsa chizwezwe.
[18] Mwa ana onse amene anabereka, panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera; mwa ana onse amene analera, panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
[19] Mavuto awiriwa akugwera iwe. Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga. Ndani angakumvere chisoni? Ndani angakutonthoze?
[20] Ana ako akomoka; ali lambalamba pa msewu, ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde. Ukali wa Yehova ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
[21] Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika, iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
[22] Ambuye Yehova wanu, Mulungu amene amateteza anthu ake akuti, “Taona, ndachotsa mʼdzanja lako chikho chimene chimakuchititsa kudzandira; sudzamwanso chikho cha ukali wanga.
[23] Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza, amene ankakuwuza kuti, ‘gona pansi tikuyende pa msana.’ Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo, ngati msewu woti ayendepo.”