Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:27

[1] Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.

[2] Tsiku limenelo Yehova adzati, “Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:

[3] Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira; ndimawuthirira nthawi zonse. Ndimawulondera usana ndi usiku kuti wina angawononge.

[4] Ine sindinakwiye. Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo! Ndikachita nazo nkhondo; ndikanazitentha zonse ndi moto.

[5] Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze; apangane nane za mtendere, ndithu, apangane nane za mtendere.”

[6] Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu, Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa, ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.

[7] Kodi Yehova anakantha Israeli ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli? Kapena kodi Yehova anapha Israeli ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?

[8] Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo, mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa, monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.

[9] Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo. Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja, ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha. Sipadzapezekanso mafano a Asera kapena maguwa ofukiza lubani.

[10] Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja, wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu; kumeneko amadyetselako ana angʼombe kumeneko zimapumulako ziweto ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.

[11] Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni. Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru; kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni, ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.

[12] Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.

[13] Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.

Yesaya — Chapters