[1] Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve: tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse: Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
[2] Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse; wapsera mtima magulu awo onse ankhondo. Iye adzawawononga kotheratu, nawapereka kuti aphedwe.
[3] Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja, mitembo yawo idzawola ndi kununkha; mapiri adzafiira ndi magazi awo.
[4] Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala; nyenyezi zonse zidzayoyoka ngati masamba ofota a mphesa, ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
[5] Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba; taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu, anthu amene ndawawononga kotheratu.”
[6] Lupanga la Yehova lakhuta magazi, lakutidwa ndi mafuta; magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi, mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna. Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
[7] Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati, ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe. Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
[8] Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira ndi kulanga adani a Ziyoni.
[9] Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula, ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule; dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
[10] Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana; utsi wake udzafuka kosalekeza. Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado; palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
[11] Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu; amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo. Mulungu adzatambalitsa pa Edomu chingwe choyezera cha chisokonezo ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
[12] Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko; akalonga ake onse adzachotsedwa.
[13] Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa, khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake. Ankhandwe azidzadya mʼmenemo; malo okhalamo akadzidzi.
[14] Avumbwe adzakumana ndi afisi, ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana. Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa ndi kupeza malo opumulirako.
[15] Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira, adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake; akamtema adzasonkhananso kumeneko, awiriawiri.
[16] Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga: mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa; sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Yehova walamula kuti zitero, ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
[17] Yehova wagawa dziko lawo; wapatsa chilichonse chigawo chake. Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.