Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:50

[1] Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu; Iye adzasakaza maonekedwe ake ndi kumwaza anthu ake onse.

[2] Aliyense zidzamuchitikira mofanana: wansembe chimodzimodzi munthu wamba, antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna, antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi, wogula chimodzimodzi wogulitsa, wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa, okongola chimodzimodzi okongoza.

[3] Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu ndi kusakazikiratu. q4 Yehova wanena mawu awa.

[4] Dziko lapansi likulira ndipo likufota, dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma, anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.

[5] Anthu ayipitsa dziko lapansi; posamvera malangizo ake; pophwanya mawu ake ndi pangano lake lamuyaya.

[6] Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi; anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo, iwo asakazika ndipo atsala ochepa okha.

[7] Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota; onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.

[8] Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha, phokoso la anthu osangalala latha, zeze wosangalatsa wati zii.

[9] Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo; akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.

[10] Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka; nyumba iliyonse yatsekedwa.

[11] Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo; chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.

[12] Mzinda wasanduka bwinja zipata zake zagumuka.

[13] Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi ndiponso pakati pa mitundu ya anthu. Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa, kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.

[14] Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe; anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.

[15] Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova; ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.

[16] Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda “Wolungamayo.” Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo, inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”

[17] Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje ndi msampha zikukudikirani.

[18] Aliyense wothawa phokoso la zoopsa adzagwa mʼdzenje; ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzakodwa ndi msampha. Zitseko zakumwamba zatsekulidwa, ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.

[19] Dziko lapansi lathyokathyoka, ndipo lagawika pakati, dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.

[20] Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba; lalemedwa ndi machimo ake. Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.

[21] Tsiku limenelo Yehova adzalanga amphamvu a kumwamba ndiponso mafumu apansi pano.

[22] Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi ngati amʼndende amene ali mʼdzenje. Adzawatsekera mʼndende ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.

[23] Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira; pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.

Yesaya — Chapters