[1] Anthu a ku Mowabu atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa, kuchokera ku Sela kudutsa chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
[2] Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku akazimwaza mʼchisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
[3] Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti, “Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite. Inu mutiteteze kwa adani anthu. Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo. Mutibise, musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
[4] Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu; mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.” Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso, kuwononga kudzaleka; waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
[5] Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi; mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
[6] Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.
[7] Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri; iwo akulirira dziko lawo. Akubuma momvetsa chisoni chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
[8] Minda ya ku Hesiboni yauma, minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga. Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda minda ya mpesa wabwino, imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri, mpaka kutambalalira ku chipululu. Mizu yake inakafika mpaka ku tsidya la nyanja.
[9] Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri, chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali, ndikukunyowetsani ndi misozi! Mwalephera kupeza zokolola, chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
[10] Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso; palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa; palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa, pakuti ndathetsa kufuwula.
[11] Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu, mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
[12] Ngakhale anthu a ku Mowabu apite ku malo awo achipembedzo koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe chifukwa sizidzatheka.
[13] Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu.
[14] Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”