Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:07

[1] Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,

[2] kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.

[3] Kodi mudzatani pa tsiku la chilango, pofika chiwonongeko chochokera kutali? Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?

[4] Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere, mkono wake uli chitambasulire.

[5] “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga, iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!

[6] Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu, ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine, kukafunkha ndi kulanda chuma, ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.

[7] Koma izi si zimene akufuna kukachita, izi si zimene zili mʼmaganizo mwake; cholinga chake ndi kukawononga, kukapulula mitundu yambiri ya anthu.

[8] Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’

[9] ‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi, nanga Samariya sali ngati Damasiko?

[10] Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano, mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;

[11] nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”

[12] Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.

[13] Pakuti mfumuyo ikuti, “ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa, ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu. Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu, ndinafunkha chuma chawo; ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.

[14] Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame, ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse; palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake, kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”

[15] Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito, kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula, kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!

[16] Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu; kunyada kwa mfumuyo kudzapsa ndi moto wosazima.

[17] Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.

[18] Ankhondo ake adzawonongedwa ngati nkhalango yayikulu ndi ngati nthaka yachonde.

[19] Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.

[20] Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli, opulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzadaliranso anthu amene anawakantha, koma adzadalira Yehova, Woyerayo wa Israeli.

[21] Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.

[22] Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja, otsala okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.

[23] Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse monga momwe analamulira.

[24] Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, “Inu anthu anga okhala mu Ziyoni, musawaope Asiriya, amene amakukanthani ndi ndodo nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.

[25] Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”

[26] Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu, monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu; ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.

[27] Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu, goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu; golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa kwambiri.

[28] Adani alowa mu Ayati apyola ku Migironi; asunga katundu wawo ku Mikimasi.

[29] Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti, “Tikagona ku Geba” Rama akunjenjemera; Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.

[30] Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tchera khutu, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka!

[31] Anthu a ku Madimena akuthawa; anthu a ku Gebimu bisalani.

[32] Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu; adzagwedeza mikono yawo, kuopseza anthu a ku Ziyoni, pa phiri la Yerusalemu.

[33] Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo, mitengo yodzikweza idzadulidwa, mitengo yayitali idzagwetsedwa.

[34] Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira; Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.

Yesaya — Chapters