Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:25

[1] Nzeru inamanga nyumba yake; inayimika nsanamira zake zisanu ndi ziwiri.

[2] Inapha ziweto zake ndipo yasakaniza vinyo wake; inasakaniza vinyo wake ndi kuyala tebulo lake.

[3] Nzeruyo inatuma adzakazi ake, kuti akakhale pamwamba penipeni pa mzinda ndi kukalengeza kuti,

[4] “Aliyense amene ali munthu wamba, abwere kuno!” Kwa onse opanda nzeru inkanena kuti,

[5] “Bwerani, dzadyeni chakudya changa ndipo dzamweni vinyo amene ndakonza.

[6] Lekani zopusa zanu kuti mukhale ndi moyo; yendani njira ya nzeru yomvetsa zinthu.”

[7] Aliyense amene amayesa kukonza munthu wonyoza amadziputira minyozo; aliyense amene amadzudzula munthu woyipa amadetsa mbiri yake.

[8] Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.

[9] Ukalangiza munthu wanzeru ndiye adzapitirira kukhala wanzeru; ukaphunzitsa munthu wolungama ndiye adzawonjezera kuphunzira kwake.

[10] Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

[11] Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo zaka za moyo wako zidzawonjezeredwa.

[12] Ngati ndiwe wanzeru, nzeru yakoyo idzakupindulitsa; ngati ndiwe wonyoza ena, udzavutika wekha.

[13] Uchitsiru ndi mkazi waphokoso, wopulikira ndiponso wosadziwa zinthu.

[14] Iye amakhala pa mpando, pa khomo la nyumba yake, pamalo aatali a mu mzinda,

[15] kuti aziyitana anthu ongodutsa, amene akunka nayenda njira zawo.

[16] Amati, “Onse amene ndi anthu wamba abwere kuno,” ndipo kwa wopanda nzeru amati,

[17] “Madzi akuba ndiye amatsekemera; chakudya chodya mobisa ndi chokoma!”

[18] Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.

Miyambo — Chapters