Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:28

[1] Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi, tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,

[2] kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.

[3] Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,

[4] koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu; ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

[5] Mapazi ake amatsikira ku imfa; akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.

[6] Iye saganizirapo za njira ya moyo; njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.

[7] Tsopano ana inu, mundimvere; musawasiye mawu anga.

[8] Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo, usayandikire khomo la nyumba yake,

[9] kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena; ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,

[10] kapenanso alendo angadyerere chuma chako ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.

[11] Potsiriza pa moyo wako udzabuwula, thupi lako lonse litatheratu.

[12] Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo! Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

[13] Sindinamvere aphunzitsi anga kapena alangizi anga.

[14] Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke pakati pa msonkhano wonse.”

[15] Imwa madzi a mʼchitsime chakochako, madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.

[16] Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu? Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?

[17] Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha, osati uyigawireko alendo.

[18] Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.

[19] Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.

[20] Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?

[21] Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona, ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.

[22] Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha; zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.

[23] Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo, adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.

Miyambo — Chapters