Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:24

[1] Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro, aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.

[2] Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru; ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.

[3] Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta, mtima wake umakwiyira Yehova.

[4] Chuma chimachulukitsa abwenzi; koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.

[5] Mboni yonama sidzalephera kulangidwa; ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.

[6] Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima, ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.

[7] Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo adzamuthawa kupita kutali. Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.

[8] Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake. Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.

[9] Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.

[10] Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!

[11] Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.

[12] Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.

[13] Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.

[14] Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo; koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.

[15] Ulesi umagonetsa tulo tofa nato ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.

[16] Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake, koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.

[17] Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

[18] Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.

[19] Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango; pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.

[20] Mvera uphungu ndipo landira malangizo; pa mapeto pake udzakhala wanzeru.

[21] Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake, koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.

[22] Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.

[23] Kuopa Yehova kumabweretsa moyo; wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.

[24] Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale; koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.

[25] Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo; dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.

[26] Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake, ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.

[27] Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.

[28] Mboni yopanda pake imanyoza cholungama, ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.

[29] Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa, ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.

Miyambo — Chapters