Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:14

[1] Munthu wokonda kukhala yekha amafunafuna zomukomera yekha; iye amatsutsana ndi malangizo onse anzeru.

[2] Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.

[3] Kuyipa mtima kukabwera, manyozonso amabwera. Manyazi amabwera pamodzi ndi kunyozeka.

[4] Mawu a munthu ali ngati madzi akuya, kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wotumphuka.

[5] Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu; kapena kupondereza munthu wosalakwa.

[6] Mawu a chitsiru amautsa mkangano; pakamwa pake pamayitana mkwapulo.

[7] Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake, ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.

[8] Mawu a miseche ali ngati chakudya chokoma; amalowa mʼmimba mwa munthu.

[9] Munthu waulesi pa ntchito yake ali pachibale ndi munthu amene amawononga zinthu.

[10] Dzina la Yehova lili ngati nsanja yolimba; wolungama amathawiramo napulumuka.

[11] Chuma cha anthu olemera chili ngati mzinda wake wolimba; chili ngati khoma lalitali limene amaganiza kuti limutchinjiriza.

[12] Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

[13] Ukayankha usanamvetse bwino nkhani, umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.

[14] Mtima wa munthu utha kupirira pa matenda, koma munthu akataya mtima ndani angathe kumulimbitsanso.

[15] Munthu wanzeru amawonjezera nzeru zina; amafunafuna kudziwa bwino zinthu.

[16] Mphatso ya munthu imamutsekulira njira yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.

[17] Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wolungama ndiye mpaka mnzake atabwera ndi kumufunsa bwino.

[18] Kuchita maere kumathetsa mikangano; amalekanitsa okangana amphamvu.

[19] Mʼbale amene wamuthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumatsekereza thandizo.

[20] Munthu amapeza bwino malingana ndi zoyankhula zake. Adzakhuta ndi zipatso za pakamwa pake.

[21] Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.

[22] Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.

[23] Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali.

[24] Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.

Miyambo — Chapters