Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:41

[1] Mwana wanga, usayiwale malangizo anga, mtima wako usunge malamulo anga.

[2] Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka ndipo udzakhala pa mtendere.

[3] Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.

[4] Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu.

[5] Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

[6] Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

[7] Usamadzione ngati wa nzeru. Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.

[8] Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino ndi mafupa ako adzakhala olimba.

[9] Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.

[10] Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.

[11] Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.

[12] Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

[13] Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

[14] pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.

[15] Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.

[16] Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.

[17] Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.

[18] Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.

[19] Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.

[20] Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka ndiponso mitambo inagwetsa mvula.

[21] Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino. Zimenezi zisakuchokere.

[22] Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.

[23] Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu, ndipo phazi lako silidzapunthwa;

[24] pamene ugona pansi, sudzachita mantha; ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.

[25] Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,

[26] pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.

[27] Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.

[28] Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.

[29] Usamukonzere chiwembu mnansi wako, amene anakhala nawe pafupi mokudalira.

[30] Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa pamene iye sanakuchitire zoyipa.

[31] Usachite naye nsanje munthu wachiwawa kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.

[32] Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa koma amayanjana nawo anthu olungama.

[33] Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa, koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.

[34] Anthu onyoza, Iye amawanyoza, koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.

[35] Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.

Miyambo — Chapters