Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:26

[1] Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola; aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.

[2] Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango; amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.

[3] Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano, koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.

[4] Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera; kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.

[5] Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya, munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.

[6] Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo, koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?

[7] Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.

[8] Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.

[9] Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga; ndilibe tchimo lililonse?”

[10] Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.

[11] Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake, ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.

[12] Makutu amene amamva ndi maso amene amaona, zonsezi anazilenga ndi Yehova.

[13] Usakonde tulo ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.

[14] Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.” Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.

[15] Pali golide ndi miyala yamtengowapatali, koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.

[16] Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole; kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.

[17] Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.

[18] Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu; ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.

[19] Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi. Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.

[20] Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake, moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.

[21] Cholowa chochipeza mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.

[22] Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!” Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.

[23] Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.

[24] Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova, tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?

[25] Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,” popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.

[26] Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu anthu oyipa.

[27] Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova; imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.

[28] Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu; chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.

[29] Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo, imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.

[30] Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa, ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.

Miyambo — Chapters