[1] Zolinga za mu mtima ndi za munthu, koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.
[2] Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake, koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.
[3] Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
[4] Yehova amachita zonse ndi cholinga chake, ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.
[5] Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.
[6] Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.
[7] Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova, ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.
[8] Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.
[9] Mtima wa munthu umalingalira zochita, koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.
[10] Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu; ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.
[11] Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.
[12] Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.
[13] Mawu owona amakondweretsa mfumu. Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.
[14] Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa, koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.
[15] Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo; ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.
[16] Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.
[17] Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa; wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.
[18] Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.
[19] Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.
[20] Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino, ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.
[21] A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu, ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.
[22] Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.
[23] Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru, ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.
[24] Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.
[25] Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.
[26] Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira; njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.
[27] Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.
[28] Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano, ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.
[29] Munthu wandewu amakopa mnansi wake, ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.
[30] Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota; amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.
[31] Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero; munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.
[32] Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.
[33] Maere amaponyedwa pa mfunga, koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.