Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:37

[1] Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.

[2] Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.

[3] Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.

[4] Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo, koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.

[5] Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake, koma wochenjera amasamala chidzudzulo.

[6] Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.

[7] Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru; koma mitima ya zitsiru sitero.

[8] Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.

[9] Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.

[10] Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Odana ndi chidzudzulo adzafa.

[11] Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova, nanji mitima ya anthu!

[12] Wonyoza sakonda kudzudzulidwa; iye sapita kwa anthu anzeru.

[13] Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe, koma mtima wosweka umawawitsa moyo.

[14] Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.

[15] Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.

[16] Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.

[17] Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi, kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.

[18] Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano, koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.

[19] Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga, koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.

[20] Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.

[21] Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.

[22] Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.

[23] Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.

[24] Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo kuti apewe malo okhala anthu akufa.

[25] Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.

[26] Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.

[27] Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.

[28] Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.

[29] Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.

[30] Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.

[31] Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo adzakhala pakati pa anthu anzeru.

[32] Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha, koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.

[33] Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.

Miyambo — Chapters