Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:32

[1] Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa, koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.

[2] Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri, koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.

[3] Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.

[4] Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa, koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.

[5] Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama, koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.

[6] Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

[7] Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu, koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.

[8] Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.

[9] Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

[10] Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa adzagwera mu msampha wake womwe, koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.

[11] Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.

[12] Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu; koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.

[13] Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.

[14] Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse, koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.

[15] Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.

[16] Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.

[17] Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.

[18] Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.

[19] Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.

[20] Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.

[21] Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.

[22] Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.

[23] Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.

[24] Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.

[25] Munthu wadyera amayambitsa mikangano, koma amene amadalira Yehova adzalemera.

[26] Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.

[27] Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

[28] Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala, koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.

Miyambo — Chapters