Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:05

[1] Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,

[2] ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;

[3] ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,

[4] ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,

[5] ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.

[6] Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru, ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.

[7] Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo. Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,

[8] pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama. Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.

[9] Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo, kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.

[10] Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako, kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.

[11] Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga; kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.

[12] Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa, kwa anthu amabodza,

[13] amene amasiya njira zolungama namayenda mʼnjira zamdima,

[14] amene amakondwera pochita zoyipa namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.

[15] Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota, ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.

[16] Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,

[17] amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.

[18] Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa; njira zake zimamufikitsa ku manda.

[19] Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera kapena kupezanso njira zamoyo.

[20] Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino, uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.

[21] Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;

[22] Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo, ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.

Miyambo — Chapters