Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:37

[1] Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga, amene anayamwa mawere a amayi anga! Ndikanakumana nawe pa njira, ndikanakupsompsona, ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.

[2] Ndikanakutenga ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, amayi amene anandiphunzitsa, ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, zotsekemera za makangadza.

[3] Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.

[4] Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani: musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Abwenzi

[5] Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Mkazi Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.

[6] Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu.

[7] Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Abwenzi

[8] Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono, koma alibe mawere, kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu pa tsiku limene adzamufunsire?

[9] Ngati iye ndi khoma, tidzamumangira nsanja ya siliva. Ngati iye ndi chitseko, tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza. Mkazi

[10] Ine ndili ngati khoma, ndipo mawere anga ndi nsanja zake. Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa ndine wobweretsa mtendere.

[11] Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni; iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi, aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.

[12] Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000 ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo. Mwamuna

[13] Iwe amene umakhala mʼminda uli pamodzi ndi anzako, ndilole kuti ndimve liwu lako! Mkazi

[14] Fulumira wokondedwa wanga, ndipo ukhale ngati gwape kapena mwana wa mbawala wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.

Nyimbo ya Solomoni — Chapters