Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:20

[1] Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse. Mkazi

[2] Undipsompsone ndi milomo yako chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.

[3] Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino; dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa. Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!

[4] Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire! Mfumu indilowetse mʼchipinda chake. Abwenzi Ife timasangalala ndi kukondwera nawe, tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo. Mkazi Amachita bwinotu potamanda iwe!

[5] Ndine wakuda, komatu ndine wokongola, inu akazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara, ngati makatani a tenti ya Solomoni.

[6] Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda, ndine wakuda chifukwa cha dzuwa. Alongo anga anandikwiyira ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa; munda wangawanga sindinawusamalire.

[7] Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana. Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere pambali pa ziweto za abwenzi ako? Abwenzi

[8] Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena, ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa ndipo udyetse ana ambuzi pambali pa matenti a abusa. Mwamuna

[9] Iwe bwenzi langa, uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.

[10] Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo, khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.

[11] Tidzakupangira ndolo zagolide zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva. Mkazi

[12] Pamene mfumu inali pa malo ake odyera, mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.

[13] Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine, kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.

[14] Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira, ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi. Mwamuna

[15] Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe chiphadzuwa, maso ako ali ngati nkhunda. Mkazi

[16] Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri! Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira. Mwamuna

[17] Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza, phaso lake ndi la mtengo wa payini.

Nyimbo ya Solomoni — Chapters