[1] Ine ndine duwa la ku Saroni, duwa lokongola la ku zigwa. Mwamuna
[2] Monga duwa lokongola pakati pa minga ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana. Mkazi
[3] Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
[4] Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
[5] Undidyetse keke ya mphesa zowuma, unditsitsimutse ndi ma apulosi, pakuti chikondi chandifowoketsa.
[6] Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
[7] Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho.
[8] Tamverani bwenzi langa! Taonani! Uyu akubwera apayu, akulumphalumpha pa mapiri, akujowajowa pa zitunda.
[9] Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera.
[10] Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine, “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
[11] Ona, nyengo yozizira yatha; mvula yatha ndipo yapitiratu.
[12] Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu.
[13] Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira; mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga tiye tizipita.” Mwamuna
[14] Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe, mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri, onetsa nkhope yako, nʼtamvako liwu lako; pakuti liwu lako ndi lokoma, ndipo nkhope yako ndi yokongola.
[15] Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa. Mkazi
[16] Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake; amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola.
[17] Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.