[1] Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti kuti timufunefune pamodzi ndi iwe? Mkazi
[2] Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake, ku timinda ta zokometsera zakudya, akukadyetsa ziweto zake ku minda, ndiponso akuthyola maluwa okongola.
[3] Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola. Mwamuna
[4] Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza, wokongola kwambiri ngati Yerusalemu, ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.
[5] Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
[6] Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa, iliyonse ili ndi ana amapasa, palibe imene ili yokha.
[7] Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu, masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.
[8] Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60, ndi azikazi 80, ndi anamwali osawerengeka;
[9] koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda. Abwenzi
[10] Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha, wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja? Mwamuna
[11] Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
[12] Ndisanazindikire kanthu, ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga. Abwenzi
[13] Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami; bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe! Mwamuna Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami, pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?