Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:51

[1] Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola mu nsapato wavalazo! Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali, ntchito ya manja ya mmisiri waluso.

[2] Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo. Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu utazunguliridwa ndi maluwa okongola.

[3] Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala, ngati mphoyo zamapasa.

[4] Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyangʼana ku Damasiko.

[5] Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli. Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu; mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.

[6] Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!

[7] Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.

[8] Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa; ndidzathyola zipatso zake.” Mawere ako ali ngati maphava a mphesa, fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,

[9] ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri. Mkazi Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga, ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.

[10] Wokondedwayo ine ndine wake, ndipo chilakolako chake chili pa ine.

[11] Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi, tikagone ku midzi.

[12] Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa, tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira, ngati maluwa ake ayamba kuoneka, komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa. Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.

[13] Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino, ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma, zatsopano ndi zakale zomwe, zimene ndakusungira wokondedwa wanga.

Nyimbo ya Solomoni — Chapters