[1] Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
[2] Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene, zochokera kozisambitsa kumene. Iliyonse ili ndi ana amapasa; palibe imene ili yokha.
[3] Milomo yako ili ngati mbota yofiira; pakamwa pako ndi pokongola kwambiri. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.
[4] Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo.
[5] Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala, ngati ana amapasa a nswala amene akudya pakati pa maluwa okongola.
[6] Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, ndidzapita ku phiri la mure ndi ku chitunda cha lubani.
[7] Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe.
[8] Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga, tiye tichoke ku Lebanoni, utsikepo pa msonga ya Amana, kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni, kuchoka ku mapanga a mikango ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
[9] Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
[10] Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
[11] Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
[12] Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa; ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.
[13] Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza; muli zipatso zokoma kwambiri, muli hena ndi nadi,
[14] nadi ndi safiro, kalamusi ndi sinamoni, komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino. Mulinso mure ndi aloe ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.
[15] Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda, chitsime cha madzi oyenda, mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni. Mkazi
[16] Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.