Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:00

[1] Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu.

[2] Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe.

[3] Mukanali adziko lapansi. Pakuti pakati panu pali kaduka ndi kukangana, kodi si inu a dziko lapansi? Kodi simukuchita ngati anthu wamba?

[4] Pamene wina anena kuti, “Ine ndimatsatira Paulo,” ndipo wina akuti, “Ine ndimatsatira Apolo,” Kodi si inu akunja?

[5] Ndiponso kodi Apolo ndi ndani? Nanga Paulo ndi ndani? Otumikira chabe, omwe kudzera mwa iwo inu munakhulupirira monga Ambuye anawagawira aliyense ntchito yake.

[6] Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa.

[7] Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu.

[8] Munthu wodzala ndi munthu wothirira ali ndi cholinga chimodzi, ndipo aliyense adzapatsidwa mphotho molingana ndi ntchito yake.

[9] Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; inu ndinu munda wa Mulungu, Nyumba ya Mulungu.

[10] Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira.

[11] Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu.

[12] Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu,

[13] ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense.

[14] Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake.

[15] Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

[16] Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?

[17] Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.

[18] Choncho musadzinyenge. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru pa mulingo wa mʼbado uno, ayenera kukhala “wopusa” kuti athe kukhala wanzeru.

[19] Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,”

[20] ndiponso, “Ambuye amadziwa kuti maganizo a wanzeru ndi opandapake.”

[21] Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu,

[22] kaya Paulo kapena Apolo kapena Kefa kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena tsopano, kapena mʼtsogolo, zonse ndi zanu,

[23] ndipo inu ndinu a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters