Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:53

[1] Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera.

[2] Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu.

[3] Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.

[4] Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira.

[5] Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.

[6] Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi.

[7] Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

[8] Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.

[9] Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe.

[10] Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha.

[11] Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya.

[12] Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.

[13] Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters