Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:10

[1] Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite.

[2] Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha.

[3] Pamenepo, ndikadzafika, ndidzawapatsa makalata a umboni anthu amene mudzawasankhe ndi kuwatuma kuti akapereka mphatso zanu ku Yerusalemu.

[4] Ngati kutaoneka kuti nʼkoyenera kuti ndipite nawo, adzapita nane limodzi.

[5] Ndidzafika kwanuko nditadutsa ku Makedoniya pakuti ndikuyembekezera kudzera ku Makedoniyako.

[6] Mwina ndidzakhala nanu kanthawi kochepa kapenanso nyengo yonse yozizira, kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite.

[7] Sindikufuna kuti ndikuoneni tsopano mongodutsa chabe, koma ndikuyembekezera kudzakhala nanu kwa kanthawi, ngati Ambuye alola.

[8] Koma ndikhala ndili ku Efeso mpaka nthawi ya Pentekosite,

[9] pakuti mwayi waukulu wapezeka woti nʼkugwira ntchito yaphindu, koma pali ambiri amene akutsutsana nane.

[10] Ngati Timoteyo afike kwanuko, onetsetsani kuti pasakhale zina zomuchititsa mantha pamene ali pakati panu, pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye monga ine.

[11] Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.

[12] Tsono kunena za mʼbale wathu, Apolo, ndinamuwumiriza kwambiri kuti abwere kwa inu abale, ndipo iye sanafune kupita tsopano. Koma akadzapeza mpata wabwino adzabwera.

[13] Khalani tcheru; khazikikani mʼchikhulupiriro chanu; limbani mtima; khalani amphamvu.

[14] Chitani zonse mwachikondi.

[15] Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale,

[16] kuti muziwamvera anthu oterewa, ndiponso aliyense wogwira nawo ntchitoyi modzipereka.

[17] Ndikondwera kuti Stefano, Fortunato ndi Akayiko afika, chifukwa akhala akundithandiza pakuti inu simuli nane.

[18] Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu womwe. Anthu a mtundu oterewa ngofunika kuwalemekeza.

[19] Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni.

[20] Abale onse kuno akupereka moni wawo. Patsanani moni wachikondi chenicheni.

[21] Ineyo Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa mawu awa akuti moni.

[22] Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!

[23] Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu.

[24] Chikondi changa chikhale ndi nonsenu mwa Khristu Yesu.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters