Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:30

[1] Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu.

[2] Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula.

[3] Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

[4] Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo.

[5] Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo.

[6] Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.

[7] Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.

[8] Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso.

[9] Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo.

[10] Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo.

[11] Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.

[12] Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.

[13] Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi mʼthupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo.

[14] Tsopano thupi silinapangidwe ndi chiwalo chimodzi koma ndi ziwalo zambiri.

[15] Ngati phazi litanena kuti, “Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi.

[16] Ndipo ngati khutu litanena kuti, “Pakuti sindine diso, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse khutu kuti lisakhale chiwalo cha thupi.

[17] Kodi thupi lonse likanakhala diso, tikanamamva bwanji? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, tikanamanunkhiza bwanji?

[18] Koma zoona nʼzakuti, Mulungu anayika ziwalo mʼthupi, chilichonse monga momwe Iye anafunira.

[19] Nanga zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, ndiye thupi likanakhala lotani?

[20] Mmene zililimu, pali ziwalo zambiri koma thupi ndi limodzi lokha.

[21] Diso silingawuze dzanja kuti, “Iwe sindikukufuna!” Ndipo mutu sungawuze phazi kuti “Iwe sindikukufuna!”

[22] Mʼmalo mwake, ziwalo zathupi zimene zimaoneka ngati zofowoka ndizo zili zofunikira kwambiri,

[23] ndipo ziwalo zathupi zimene timaziyesa zopanda ulemu, ndizo timazilemekeza kwambiri. Ndipo ziwalo zosaoneka bwino ndizo zimalandira ulemu wapadera.

[24] Koma ziwalo zooneka bwino, nʼkosafunika kuti tizisamalire mwapadera. Mulungu polumikiza ziwalo zathupi, anapereka ulemu wopambana kwa ziwalo zimene zimafunadi ulemuwo

[25] kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane.

[26] Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

[27] Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.

[28] Ndipo Mulungu mu mpingo anayika poyamba atumwi, kachiwiri aneneri, kachitatu aphunzitsi, kenaka ochita zozizwitsa, ena a mphatso zamachiritso, ena a mphatso yothandiza anzawo, ena a mphatso yotsogolera ndiponso ena a mphatso ya malilime.

[29] Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse amachita zozizwitsa?

[30] Kodi onse ali ndi mphatso zamachiritso? Kodi onse amayankhula malilime? Kodi onse amatanthauzira malilime?

[31] Koma funitsitsani mphatso zopambana. Tsopano ndikuonetsani njira yopambana kwambiri.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters