Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 7:53

[1] Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri.

[2] Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi.

[3] Koma amene amanenera amayankhula kwa anthu kuti awapatse mphamvu, awalimbikitse ndi kuwakhazikitsa mtima pansi.

[4] Iye amene amayankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma amene amanenera amalimbikitsa mpingo.

[5] Nʼkanakonda kuti aliyense mwa inu atamayankhula malilime, koma ndi bwino kuti muzinenera. Amene amanenera amaposa amene amayankhula malilime, pokhapokha atatanthauzira kuti mpingo upindule.

[6] Tsono, abale, mudzapindula chiyani nditabwera kwa inu ndi kukuyankhulani mʼmalilime? Koma mudzapindula ngati nditakubweretserani vumbulutso lina lake, kapena chidziwitso, kapena chiphunzitso.

[7] Ngakhale mu zinthu zopanda moyo monga chitoliro kapena gitala, zimene zimatulutsa liwu; kodi munthu akhoza kudziwa bwanji nyimbo imene ikuyimbidwa ngati mawu sakumveka mogwirizana bwino?

[8] Komanso ngati lipenga silimveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo?

[9] Chimodzimodzinso inu. Ngati simungayankhule mawu omveka bwino mʼchiyankhulo chanu, wina angadziwe bwanji chimene mukunena? Muzingodziyankhulira nokha.

[10] Mosakayika, pali ziyankhulo zosiyanasiyana pa dziko lapansi, koma palibe nʼchimodzi chomwe chimene chilibe tanthauzo.

[11] Tsono ngati sindingatolepo tanthauzo la zimene wina akuyankhula, ndiye kuti ndine mlendo kwa oyankhulayo ndipo iyeyo ndi mlendo kwa ine.

[12] Chimodzimodzinso inu. Popeza mumafunitsitsa mphatso za Mzimu, yesetseni kuchita bwino pa mphatso zimene zimamanga mpingo.

[13] Pa chifukwa ichi munthu amene amayankhula malilime apemphere kuti azitha kutanthauzira zimene akunena.

[14] Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu.

[15] Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga.

[16] Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena?

[17] Mukhoza kumathokoza mokwanira, koma munthu winayo sanathandizikepo.

[18] Ndikuyamika Mulungu chifukwa ndimayankhula malilime kuposa nonsenu.

[19] Koma mu mpingo ndi kwabwino kuti ndiyankhule mawu asanu okha omveka bwino kuti ndilangize bwino ena kusiyana ndikuyankhula mawu ambirimbiri mʼmalilime.

[20] Abale, lekani kuganiza ngati ana. Mukhale ana pa nkhani ya zoyipa koma mʼmaganizo anu mukhale okhwima.

[21] Zinalembedwa mʼMalamulo kuti, “Ndidzayankhula kwa anthu awa, kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo ndiponso ndi milomo yachilendo. Koma ngakhale nthawi imeneyo sadzandimvera Ine, q4 akutero Ambuye.”

[22] Kotero, malilime ndi chizindikiro, osati cha kwa okhulupirira koma kwa osakhulupirira. Koma kunenera ndi chizindikiro kwa okhulupirira osati kwa osakhulupirira.

[23] Kotero kuti ngati mpingo wonse utasonkhana pamodzi ndipo aliyense namayankhula malilime, ndipo wina amene sangazindikire kapena ena osakhulupirira nabwerapo, kodi sadzanena kuti mwachita misala?

[24] Koma ngati wosakhulupirira kapena wina amene sakuzindikira abwera pamene aliyense akunenera, adzatsutsika mu mtima ndi zonse zimene akumva ndipo adzaweruzidwa ndi onse

[25] ndipo zinsinsi za mu mtima mwake zidzawululika. Kotero kuti adzadzigwetsa pansi ndi kupembedza Mulungu akufuwula kuti, “Mulungu ali pakati panudi!”

[26] Kodi tsono abale, tinene chiyani? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense amakhala ali ndi nyimbo yoti ayimbe, kapena mawu oti alangize, vumbulutso, malilime, kapena kumasulira kwake. Zonsezi cholinga chake chikhale kulimbikitsa mpingo.

[27] Ngati wina ayankhula malilime, awiri kapena akachulukapo atatu ndiye ayankhule mmodzimmodzi, ndipo wina ayenera kutanthauzira zimene ayankhulazo.

[28] Ngati palibe wotanthauzira, woyankhulayo akhale chete mu mpingo ndipo adziyankhulire iye mwini ndi Mulungu.

[29] Aneneri awiri kapena atatu anenere, ndipo enawo asanthule mosamalitsa zimene anenerazo.

[30] Ndipo ngati vumbulutso labwera kwa munthu amene wakhala pansi, amene akuyankhulayo akhale chete.

[31] Pakuti nonse mukhoza kunenera mmodzimmodzi motsatana kuti aliyense alangizidwe ndi kulimbikitsidwa.

[32] Mizimu ya aneneri imamvera ulamuliro wa aneneri.

[33] Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo koma wamtendere. Monga mwa mipingo yonse ya oyera mtima.

[34] Amayi akhale chete mʼmisonkhano ya mpingo. Iwo asaloledwe kuyankhula, koma azikhala omvera monga mmene lamulo linenera.

[35] Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna awo ku nyumba. Nʼchochititsa manyazi kuti mkazi ayankhule mu msonkhano wa mpingo.

[36] Kodi kapena mawu a Mulungu anachokera kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?

[37] Ngati wina aliyense akuganiza kuti ndi mneneri kapena kuti ali ndi mphatso za Mzimu, ayenera kudziwa kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo la Ambuye.

[38] Ngati munthu savomereza zimenezi, iyeyonso sadzavomerezedwa.

[39] Nʼchifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse anthu kuyankhula malilime.

[40] Koma chilichonse chichitike moyenera ndi mwadongosolo.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters