Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:49

[1] Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu.

[2] Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo.

[3] Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri.

[4] Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu,

[5] kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.

[6] Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha.

[7] Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi.

[8] Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero.

[9] Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

[10] koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake. Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.

[11] Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo.

[12] Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.

[13] Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu.

[14] Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.

[15] Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense.

[16] Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu.

Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Akorinto — Chapters