[1] Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda.
[2] Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika
[3] ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu.
[4] Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo.
[5] Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa?
[6] Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya:
[7] ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ”
[8] Ndipo anakumbukira mawu ake.
[9] Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse.
[10] Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi.
[11] Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru.
[12] Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
[13] Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu.
[14] Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo.
[15] Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi;
[16] koma iwo sanamuzindikire.
[17] Iye anawafunsa kuti,“Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa.
[18] Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, “Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?”
[19] Iye anafunsa kuti,“Zinthu zotani?” Iwo anayankha nati, “Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
[20] Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye;
[21] koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi.
[22] Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa
[23] koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo.
[24] Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone.”
[25] Iye anawawuza kuti,“Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!
[26] Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?”
[27] Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
[28] Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira.
[29] Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, “Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa.” Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
[30] Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira.
[31] Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo.
[32] Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”
[33] Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi
[34] ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.”
[35] Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.
[36] Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati,“Mukhale ndi mtendere.”
[37] Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa.
[38] Iye anawafunsa kuti,“Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?
[39] Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
[40] Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake.
[41] Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti,“Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?”
[42] Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika.
[43] Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.
[44] Iye anawawuza kuti,“Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
[45] Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.
[46] Iye anawawuza kuti,“Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu.
[47] Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu.
[48] Inu ndinu mboni za zimenezi.
[49] Ine ndidzakutumizirani chimene Atate anga analonjeza. Koma khalani mu mzinda muno mpaka mutavekedwa mphamvu yochokera kumwamba.”
[50] Iye atawatengera kunja kwa mzindawo mpaka ku Betaniya, anakweza manja ake ndi kuwadalitsa.
[51] Iye akuwadalitsa, anawasiya ndipo anatengedwa kupita kumwamba.
[52] Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu.
[53] Ndipo iwo anakhalabe ku Nyumba ya Mulungu, akulemekeza Mulungu.