Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 9:35

[1] Kenaka gulu lonse la anthuwo linayimirira ndi kumutengera kwa Pilato.

[2] Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”

[3] Pamenepo Pilato anamufunsa Yesu kuti, “Kodi Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti,“Mwatero ndinu.”

[4] Kenaka Pilato anawawuza akulu a ansembe ndi gulu la anthu, “Ine sindikumupeza cholakwa munthuyu.”

[5] Koma iwo analimbikirabe kuti, “Iyeyu amasokoneza anthu ku Yudeya konse ndi chiphunzitso chake, Iyeyu anayambira ku Galileya ndipo wayenda mtunda wonse mpaka kuno.”

[6] Pakumva zimenezi, Pilato anafunsa ngati munthuyo ndi Mgalileya.

[7] Iye atamva kuti Yesu anali pansi pa ulamuliro wa Herode, anamutumiza kwa Herodeyo, amene pa nthawi imeneyo analinso mu Yerusalemu.

[8] Herode ataona Yesu, anakondwa kwambiri, chifukwa kwa nthawi yayitali, ankafunitsitsa atamuona. Kuchokera pa zimene anamva za Iye, anayembekezera kuti achita zodabwitsa.

[9] Iye anamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sanayankhe.

[10] Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anayimirira pamenepo ndi kumuneneza kwambiri.

[11] Pamenepo Herode ndi asilikali ake anamuseka ndi kumunyoza Iye. Atamuveka mkanjo wonyezimira, anamutumizanso kwa Pilato.

[12] Tsiku limenelo, Herode ndi Pilato anakhala abwenzi. Zisanachitike izi anali adani.

[13] Pilato anasonkhanitsa akulu a ansembe, oweruza ndi anthu,

[14] ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.

[15] Herodenso sanapeze chifukwa pakuti wamutumizanso kwa ife monga mmene mukuoneramu. Iyeyu sanachite chinthu chakuti aphedwe.

[16] Nʼchifukwa chake, ine ndingomulanga, nʼkumumasula.”

[17] (Pa nthawi yachikondwerero cha Paska iye ankayenera kumasula munthu mmodzi).

[18] Onse pamodzi anafuwula kuti, “Muchotseni munthuyu! Timasulireni Baraba!”

[19] (Baraba anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe mu mzinda ndi kupha).

[20] Pofuna kumumasula Yesu, Pilato anawadandaulira iwo.

[21] Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”

[22] Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”

[23] Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira.

[24] Choncho Pilato anatsimikiza kuchita zofuna zawozo.

[25] Iye anawamasulira munthu amene anaponyedwa mʼndende chifukwa choyambitsa chipolowe ndi kupha, amene ankamufunayo, ndipo anawapatsa Yesu mwakufuna kwawo.

[26] Ndipo pamene ankapita naye, anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera ku munda, namusenzetsa mtanda namuyendetsa pambuyo pa Yesu.

[27] Gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye, kuphatikiza amayi amene ankabuma ndi kumulirira.

[28] Yesu anatembenuka nati kwa iwo,“Ana aakazi a Yerusalemu, musandilirire Ine; dzililireni nokha ndi ana anu.

[29] Pakuti nthawi idzabwera imene inu mudzati, ‘Ndi odala amayi osabereka, mimba zimene sizinabereke ndi mawere amene sanayamwitse!’

[30] Kenaka, “adzawuza mapiri kuti tigwereni ife; zitunda kuti tiphimbeni ife.

[31] Chifukwa ngati anthu akuchita izi pa mtengo wauwisi, chidzachitike nʼchiyani ndi wowuma?”

[32] Amuna ena awiri, onsewo achifwamba, anatengedwanso pamodzi ndi Yesu kukaphedwa.

[33] Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere.

[34] Yesu anati,“Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.

[35] Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”

[36] Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa,

[37] ndipo anati, “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.”

[38] Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: .

[39] Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!”

[40] Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi?

[41] Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.”

[42] Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.”

[43] Yesu anayankha kuti,“Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”

[44] Linali tsopano pafupi ora lachisanu ndi chimodzi, ndipo mdima unagwa pa dziko lonse mpaka ora lachisanu ndi chinayi,

[45] pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.

[46] Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti,“Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.

[47] Kenturiyo, ataona zimene zinachitikazi, analemekeza Mulungu ndipo anati, “Zoonadi, uyu anali munthu wolungama.”

[48] Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka.

[49] Koma onse amene anamudziwa Iye, kuphatikiza amayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya, anayimirira akuona zinthu izi.

[50] Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama.

[51] Iye sanavomereze zimene anzake abwalo anagwirizana ndi kuchita. Iye ankachokera ku mudzi wa Arimateyu wa ku Yudeya ndipo ankayembekezera ufumu wa Mulungu.

[52] Atapita kwa Pilato, iye anakapempha mtembo wa Yesu.

[53] Ndipo anawutsitsa, nawukulunga nsalu yabafuta nawuyika mʼmanda wosemedwa mʼmwala, amene panalibe wina amene anayikidwamo.

[54] Linali tsiku lokonzekera ndipo Sabata linatsala pangʼono kuyamba.

[55] Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira.

[56] Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Luka — Chapters