[1] Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira,
[2] akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu.
[3] Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo.
[4] Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu.
[5] Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama.
[6] Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.
[7] Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe.
[8] Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati,“Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”
[9] Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”
[10] Iye anayankha kuti,“Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe,
[11] ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’
[12] Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”
[13] Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.
[14] Ora litakwana, Yesu ndi ophunzira ake anakhala pa tebulo.
[15] Ndipo Iye anawawuza kuti,“Ine ndakhala ndikuyembekezera kudya Paska uyu ndi inu ndisanamve zowawa.
[16] Pakuti Ine ndikukuwuzani kuti sindidzadyanso Paska wina mpaka Paskayi itakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu.”
[17] Atanyamula chikho, Iye anayamika ndipo anati,“Tengani ndipo patsiranani pakati panu.
[18] Pakuti ndikukuwuzani kuti, Ine sindidzamwanso zochokera ku chipatso cha mphesa mpaka ufumu wa Mulungu utabwera.”
[19] Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati,“Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
[20] Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu.
[21] Koma dzanja la amene akundipereka Ine lili pamodzi ndi langa pa chakudya pano.
[22] Mwana wa Munthu apita monga mmene zinalembedwera, koma tsoka kwa munthu amene amupereka Iye.”
[23] Iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndi ndani wa iwo amene akanachita ichi.
[24] Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu.
[25] Yesu anawawuza kuti,“Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’
[26] Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira.
[27] Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.
[28] Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero.
[29] Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine,
[30] kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
[31] “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu.
[32] Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”
[33] Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”
[34] Yesu anayankha kuti,“Ine ndikukuwuza Petro, tambala asanalire lero lino, udzandikana katatu kuti sukundidziwa Ine.”
[35] Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti,“Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?” Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.”
[36] Iye anawawuza kuti,“Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula.
[37] Zalembedwa kuti, ‘Ndipo Iye anawerengedwa pamodzi ndi anthu ochimwa,’ ndipo Ine ndikuwuzani kuti izi ziyenera kukwaniritsidwa mwa Ine. Inde, zimene zinalembedwa za Ine, zikukwaniritsidwa.”
[38] Ophunzira anati, “Taonani Ambuye, awa malupanga awiri.” Iye anayankha kuti,“Amenewa akwanira.”
[39] Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye.
[40] Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti,“Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.”
[41] Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti,
[42] “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”
[43] Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa.
[44] Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi.
[45] Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni.
[46] Iye anafunsa kuti,Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”
[47] Pamene Iye ankayankhulabe, gulu la anthu linabwera, ndipo munthu wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo analitsogolera. Iye anamuyandikira Yesu kuti amupsompsone.
[48] Koma Yesu anamufunsa kuti,“Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa Munthu ndi mpsopsono?”
[49] Otsatira Yesu ataona zimene zimati zichitike, anati, “Ambuye, kodi timenyane ndi malupanga athu?”
[50] Ndipo mmodzi wa iwo anatema wantchito wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake lamanja.
[51] Koma Yesu anayankha kuti,“Zisachitikenso zimenezi!” Ndipo Iye anakhudza khutu la munthuyo ndi kumuchiritsa.
[52] Kenaka Yesu anafunsa akulu a ansembe, akuluakulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi akuluakulu ena amene anabwerawo kuti,“Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira kuti mubwere ndi malupanga ndi zibonga?
[53] Tsiku lililonse ndinali nanu mʼmabwalo a mʼNyumba ya Mulungu ndipo inu simunandigwire. Koma iyi ndi nthawi yanu pamene mdima ukulamulira.”
[54] Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali.
[55] Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi.
[56] Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
[57] Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
[58] Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.” Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
[59] Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
[60] Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira.
[61] Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti,“Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.”
[62] Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
[63] Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya.
[64] Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?”
[65] Ndipo iwo anamunena zachipongwe zambiri.
[66] Kutacha, bungwe la akuluakulu, pamodzi ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, anakumana pamodzi, ndipo anamuyika Yesu patsogolo pawo.
[67] Iwo anati, “Tiwuze, ngati ndiwe Khristu.” Yesu anayankha kuti,“Ine nditakuwuzani simungandikhulupirire.
[68] Ine nditakufunsani inu, simungandiyankhe.
[69] Koma kuyambira tsopano, Mwana wa Munthu adzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvu.”
[70] Onse anafunsa kuti, “Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anayankha kuti,“Mwanena ndinu kuti Ndine.”
[71] Pamenepo iwo anati, “Nanga tikufuniranjinso umboni wina? Ife tamva kuchokera pa milomo yake.”