[1] Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.
[2] Iye anati,“Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu.
[3] Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’
[4] “Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu,
[5] koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”
[6] Ndipo Ambuye anati,“Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena.
[7] Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira?
[8] Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”
[9] Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse.
[10] “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho.
[11] Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu.
[12] Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’
[13] “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’
[14] “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
[15] Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula.
[16] Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati,“Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere.
[17] Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”
[18] Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
[19] Yesu anamuyankha kuti,“Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha.
[20] Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
[21] Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”
[22] Yesu atamva izi, anati kwa iye,“Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”
[23] Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri.
[24] Yesu anamuyangʼana nati,“Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!
[25] Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
[26] Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
[27] Yesu anayankha kuti,“Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
[28] Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
[29] Yesu anawawuza kuti,“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu
[30] adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”
[31] Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti,“Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa.
[32] Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira,
[33] adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”
[34] Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
[35] Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha,
[36] anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika.
[37] Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”
[38] Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
[39] Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
[40] Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti,
[41] “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”
[42] Yesu anati kwa iye,“Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.”
[43] Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.