Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 9:06

[1] Yesu analowa mu Yeriko napitirira.

[2] Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera.

[3] Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu.

[4] Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

[5] Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye,“Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.”

[6] Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

[7] Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”

[8] Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

[9] Yesu anati kwa iye,“Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu.

[10] Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

[11] Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo.

[12] Iye anati,“Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo.

[13] Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’

[14] “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’

[15] “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.

[16] “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’

[17] “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’

[18] “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’

[19] “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’

[20] “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu.

[21] Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’

[22] “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale?

[23] Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’

[24] “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”

[25] Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”

[26] Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.

[27] Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”

[28] Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu.

[29] Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo,

[30] “Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno.

[31] Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”

[32] Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira.

[33] Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?”

[34] Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.”

[35] Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu.

[36] Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.

[37] Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.

[38] “Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!” “Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”

[39] Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!”

[40] Iye anayankha kuti,“Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”

[41] Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira

[42] nati,“Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako.

[43] Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse.

[44] Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”

[45] Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda.

[46] Iye anawawuza kuti,“Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”

[47] Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe.

[48] Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake.

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Luka — Chapters