[1] Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda.
[2] Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira.
[3] Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala.
[4] Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa.
[5] Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa.
[6] Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona.
[7] Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”
[8] Pamenepo amayiwo anachoka mofulumira ku mandako ali ndi mantha komabe atadzaza ndi chimwemwe, ndipo anathamanga kukawuza ophunzira ake.
[9] Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati,“Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira.
[10] Ndipo Yesu anawawuza kuti,“Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.”
[11] Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika.
[12] Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri,
[13] nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’
[14] Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.”
[15] Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.
[16] Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite.
[17] Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika.
[18] Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati,“Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.
[19] Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,
[20] ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”