[1] Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri,
[2] nawawuza kuti,“Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine.
[3] Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.”
[4] Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:
[5] “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni, taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yofatsa ndi yokwera pa bulu, pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
[6] Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira.
[7] Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo.
[8] Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo.
[9] Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti, “Hosana Mwana wa Davide!” “Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!” “Hosana mmwambamwamba!”
[10] Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”
[11] Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.”
[12] Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.
[13] Iye anawawuza kuti,“Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”
[14] Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa.
[15] Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.
[16] Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?” Yesu anayankha nati,“Inde. Kodi simunawerenge kuti, “Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda mwatuluka mayamiko?”
[17] Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona.
[18] Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala.
[19] Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo,“Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
[20] Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”
[21] Yesu anayankha kuti,“Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.
[22] Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”
[23] Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
[24] Yesu anayankha kuti,“Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi.
[25] Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’
[26] Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”
[27] Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.” Pamenepo Iye anati,“Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”
[28] “Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
[29] “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.
[30] “Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.
[31] “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?” Anamuyankha nati, “Woyambayo.” Yesu anawawuza kuti,“Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.”
[32] Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
[33] “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo.
[34] Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.
[35] “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo.
[36] Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi.
[37] Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.
[38] “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’
[39] Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.
[40] “Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”
[41] Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”
[42] Yesu anawawuza kuti,“Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
[43] “Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake.
[44] Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”
[45] Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo.
[46] Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.