[1] Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake,
[2] “Monga mukudziwa, kwatsala masiku awiri kuti Paska ifike ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.”
[3] Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa,
[4] ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha.
[5] Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”
[6] Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate,
[7] mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.
[8] Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere?
[9] Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”
[10] Yesu podziwa izi anawawuza kuti,“Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino.
[11] Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.
[12] Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda.
[13] Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”
[14] Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe
[15] nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu.
[16] Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
[17] Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”
[18] Iye anayankha kuti,“Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ”
[19] Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska.
[20] Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya.
[21] Akudya, Iye anati,“Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka.”
[22] Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”
[23] Yesu anayankha nati,“Iye amene akusunsa mʼmbale pamodzi ndi Ine, yemweyo adzandipereka.
[24] Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
[25] Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?” Yesu anayankha nati,“Iwe watero.”
[26] Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti,“Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.”
[27] Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati,“Imwani nonsenu.
[28] Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo.
[29] Ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mtengo wa mpesa kuyambira lero mpaka tsiku ilo pamene ndidzamwenso mwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate anga.”
[30] Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.
[31] Pamenepo Yesu anawawuza kuti,“Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’
[32] Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
[33] Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”
[34] Yesu anayankha nati,“Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.”
[35] Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.
[36] Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti,“Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.”
[37] Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima.
[38] Pamenepo anawawuza kuti,“Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.”
[39] Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti,“Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”
[40] Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti,“Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha?
[41] Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”
[42] Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti,“Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”
[43] Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo.
[44] Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.
[45] Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo,“Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa.
[46] Imirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!”
[47] Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu.
[48] Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.”
[49] Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.
[50] Yesu anayankha kuti,“Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.” Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga.
[51] Pa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.
[52] Yesu anati kwa iye,“Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga.
[53] Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri?
[54] Koma nanga malemba akwaniritsidwa bwanji amene akuti ziyenera kuchitika motere?”
[55] Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo,“Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire.
[56] Koma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa.
[57] Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana.
[58] Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
[59] Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu.
[60] Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka. Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo.
[61] Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”
[62] Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?”
[63] Koma Yesu anakhalabe chete. Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.”
[64] Yesu anayankha nati,“Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.”
[65] Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake.
[66] Mukuganiza bwanji?” Iwo anayankha kuti, “Ayenera kuphedwa!”
[67] Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi.
[68] Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”
[69] Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”
[70] Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”
[71] Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”
[72] Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”
[73] Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”
[74] Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!” Nthawi yomweyo tambala analira.
[75] Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti,“Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.