Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:43

[1] Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.

[2] Iye anayankha kuti,“Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira.

[3] Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi.

[4] Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.

[5] Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi.

[6] Yesu anawawuza kuti,“Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”

[7] Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.”

[8] Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti,“Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa.

[9] Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza?

[10] Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza?

[11] Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”

[12] Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.

[13] Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti,“Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?”

[14] Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”

[15] Iye anafunsa kuti,“Nanga inuyo mumati ndine yani?”

[16] Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”

[17] Yesu anati kwa iye,“Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba.

[18] Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa.

[19] Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.”

[20] Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu.

[21] Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.

[22] Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.”

[23] Yesu anatembenuka nati kwa Petro,“Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”

[24] Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake,“Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.

[25] Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza.

[26] Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake?

[27] Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.

[28] “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”

Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Mateyu — Chapters